Ndipo pamene iwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitidwa.
Luka 8:34 - Buku Lopatulika Ndipo akuwetawo m'mene anaona chimene chinachitika, anathawa, nauza okhala mumzinda ndi kuminda. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo akuwetawo m'mene anaona chimene chinachitika, anathawa, nauza akumudzi ndi kumilaga yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Oŵeta nkhumbazo ataona zimenezi, adathaŵa, nakauza anthu ku mzinda ndi ku midzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Oweta nkhumbazo ataona zimene zinachitikazo, anathamanga ndi kukanena izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi. |
Ndipo pamene iwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitidwa.
Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mzinda, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho.
Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nkulowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa.
Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa.