Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.
Luka 8:21 - Buku Lopatulika Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawachita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawachita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yesu adati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi anthu amene amamva mau a Mulungu, nkumachitadi zimene mauwo akunena.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anayankha kuti, “Amayi ndi abale anga ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kumachita zimene mawuwo akunena.” |
Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.
Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundichitira ichi Ine.
Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko.
Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.
Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.
Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.
ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.
Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.
Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuone Mulungu.