Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.
Luka 8:20 - Buku Lopatulika Ndipo anamuuza Iye, kuti, Amai wanu ndi abale anu alinkuima kunja, nafuna kuona Inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamuuza Iye, kuti, Amai wanu ndi abale anu alinkuima kunja, nafuna kuona Inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono munthu wina adauza Yesu kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akufuna kukuwonani.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunja, akufuna kukuonani.” |
Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.
Ndipo anadza kwa Iye amake ndi abale ake, ndipo sanakhoze kumfika, chifukwa cha khamu la anthu.
Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawachita.
Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.
Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?