Luka 8:19 - Buku Lopatulika Ndipo anadza kwa Iye amake ndi abale ake, ndipo sanakhoze kumfika, chifukwa cha khamu la anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anadza kwa Iye amake ndi abale ake, ndipo sanakhoze kumfika, chifukwa cha khamu la anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako, koma chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, adaalephera kufika pamene panali Iyepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano amayi ndi abale a Yesu anabwera kudzamuona Iye, koma analephera kuti afike pafupi ndi Iye chifukwa cha gulu la anthu. |