Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.
Luka 8:16 - Buku Lopatulika Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Palibe munthu amene amayatsa nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumba aone kuŵala kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Palibe amayatsa nyale ndi kuyibisa mu mtsuko kapena kuyika pansi pa bedi. Koma mʼmalo mwake, amayika pa choyikapo chake, kuti anthu olowamo aone kuwala. |
Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.
Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.
kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.
chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.
Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikaponyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.