Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.
Luka 8:11 - Buku Lopatulika Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbeu zija ndi mau a Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu. |
Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.
Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira.
Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.
Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.