Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.
Luka 7:48 - Buku Lopatulika Ndipo anati kwa mkazi, Machimo ako akhululukidwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati kwa mkazi, Machimo ako akhululukidwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Yesu adauza mai uja kuti, “Machimo ako akhululukidwa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anati kwa mayiyo, “Machimo ako akhululukidwa.” |
Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.
Pakuti chapafupi nchiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka. Nuyende?
Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa.
Chapafupi nchiti, kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?
Chapafupi nchiti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende?
Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono.