Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.
Luka 7:46 - Buku Lopatulika Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwe sudandidzoze kumutu kwanga ndi mafuta, koma iyeyu wadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwe sunadzoze mutu wanga mafuta, koma iye wadzoza mapazi anga mafuta onunkhira. |
Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye.
Ndipo Yowabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nuvale zovala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikulu.
ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.
Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.
Chakudya chofunika osachidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu.
akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe.
Udzafesa koma osacheka; udzaponda azitona koma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo.
Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono.
Usambe tsono, nudzole, nuvale zovala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko.