Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.
Luka 7:41 - Buku Lopatulika Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ake a marupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ake a marupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Panali anthu aŵiri amene adaakongola ndalama kwa munthu wokongoza ndalama. Wina adaakongola ndalama makumi asanu, wina ndalama zisanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Anthu awiri anakongola ndalama kwa munthu wina wokongoletsa ndalama: mmodzi ndalama zokwana 500 ndi winayo ndalama makumi asanu. |
Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Israele wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga.
Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.
Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola.
Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya?
Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.
Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.
Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya mu Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu?
Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anavomera, Mphunzitsi, nenani.
Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono.
Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa;