Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.
Luka 7:34 - Buku Lopatulika Mwana wa Munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa! Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mwana wa Munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa! Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwana wa Munthu adabwera, nkumadya ndi kumwa ndithu, inu mumvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’ |
Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.
Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?
Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?
Ndipo pakulankhula Iye, anamuitana Mfarisi kuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya.
Ndipo panali pamene Iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akulu a Afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye.
Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.
Ndipo Levi anamkonzera Iye phwando lalikulu kunyumba kwake; ndipo panali khamu lalikulu la amisonkho, ndi enanso amene analikuseama pachakudya pamodzi nao.
Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi chiwanda.
Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana Iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m'nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya.
Ndipo anamkonzera Iye chakudya komweko; ndipo Marita anatumikira; koma Lazaro anali mmodzi wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye.