Luka 7:32 - Buku Lopatulika Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavine ai; tinabuma maliro, ndimo simunalire ai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavina ai; tinabuma maliro, ndimo simunalira ai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ali ngati ana okangana pa msika, ena akufunsa anzao kuti, “ ‘Tidaakuimbirani ng'oma yaukwati, bwanji inu osavina? Tidaabuma maliro, bwanji inu osalira?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti, “ ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro, koma inu simunavine. Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro, koma inu simunalire.’ |
Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi chiwanda.