Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?
Luka 7:31 - Buku Lopatulika Ndipo, ndidzafanizira ndi chiyani anthu a mbadwo uno? Ndipo afanana ndi chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo, ndidzafanizira ndi chiyani anthu a mbadwo uno? Ndipo afanana ndi chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Kaya anthu amakonoŵa ndingaŵafanizire ndi chiyani? Ali ngati chiyani? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Kodi ndingawafanizire chiyani anthu a mʼbado uno? Ali ngati chiyani? |
Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?
Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe;
Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?
Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.
Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavine ai; tinabuma maliro, ndimo simunalire ai.