Luka 7:30 - Buku Lopatulika Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Afarisi ndi akatswiri a Malamulo, pakukana kubatizidwa ndi iye, adakana okha zimene Mulungu adafuna kuŵachitira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Afarisi ndi akatswiri amalamulo anakana cholinga cha Mulungu kwa iwo okha, chifukwa sanabatizidwe ndi Yohane. |
Bwanji muti, Tili ndi nzeru ife, ndi malamulo a Yehova ali ndi ife? Koma, taona, peni lonyenga la alembi lachita zonyenga.
Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawirikawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m'mapiko ake, ndipo simunafunai!
Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.
Koma kwa Israele anena, Dzuwa lonse ndinatambalitsira manja anga kwa anthu osamvera ndi okanakana.
Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,
Sindichiyesa chopanda pake chisomo cha Mulungu; pakuti ngati chilungamo chili mwa lamulo, Khristu adafa chabe.
Mwa Iye tinayesedwa akeake olandira cholowa, popeza tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake;