Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.
Luka 7:27 - Buku Lopatulika Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye, Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere, amene adzakukonzera njira yako pamaso pako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye, Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere, amene adzakukonzera njira yako pamaso pako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, “ ‘Nayitu nthumwi yanga, ndikuituma m'tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyu ndi amene malemba akunena za Iye kuti, “ ‘Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu, amene adzakonza njira yanu.’ |
Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu.
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu.
Monga mwalembedwa mu Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu.
Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.
Koma munatuluka kukaona chiyani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo wakuposa mneneri.
Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.
Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.