Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana; chifukwa unakwera pa kama wa atate wako; pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.
Luka 7:24 - Buku Lopatulika Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amithenga a Yohane aja atachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “Kodi m'mene mudaapita ku chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu otumidwa ndi Yohane aja atachoka, Yesu anayamba kuyankhula ndi gulu la anthu za Yohaneyo kuti, “Kodi munkapita ku chipululu kukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo? |
Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana; chifukwa unakwera pa kama wa atate wako; pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.
Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.
pa ukulu wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zekariya m'chipululu.
Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zofewa kodi? Onani, iwo akuvala zolemera, ndi akukhala odyerera, ali m'nyumba za mafumu.
Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
Aphunzitsi onamawo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira.
Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.