Luka 7:23 - Buku Lopatulika Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Odala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.” |
Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;
Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.
Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?
Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sangathe kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu.