Luka 7:20 - Buku Lopatulika Ndipo pakufika kwa Iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakufika kwa Iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene iwo adafika kwa Yesu, adamuuza kuti, “Yohane Mbatizi watituma kwa Inu kuti tidzakufunseni kuti, ‘Kodi Inuyo ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthuwo atafika kwa Yesu anati, “Yohane Mʼbatizi watituma kwa Inu kuti tidzafunse kuti, ‘Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?’ ” |
Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?
Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.