Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,
Luka 7:17 - Buku Lopatulika Ndipo mbiri yake imeneyo inabuka ku Yudeya yense, ndi ku dziko lonse loyandikira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mbiri yake imeneyo inabuka ku Yudeya lonse, ndi ku dziko lonse loyandikira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbiri ya Yesuyi idawanda m'dziko lonse la Yudeya, ndi ku madera onse ozungulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbiriyi inafalikira ku Yudeya konse ndi ku madera ozungulira. |
Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.
Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.
Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.