Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili.
Luka 7:15 - Buku Lopatulika Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo wakufayo adakhala tsonga nayamba kulankhula, Yesu nkumupereka kwa mai wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wakufayo anakhala tsonga ndi kuyamba kuyankhula, ndipo Yesu anamupereka mnyamatayo kwa amayi ake. |
Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili.
Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.
Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.