Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.
Luka 7:10 - Buku Lopatulika Ndipo pakubwera kunyumba otumidwawo, anapeza kapoloyo wachira ndithu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakubwera kunyumba otumidwawo, anapeza kapoloyo wachira ndithu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Otumidwa aja adabwerera kunyumba, nakapeza wantchito uja atachiritsidwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anthu amene anatumidwawo anabwerera ku nyumba ndipo anakamupeza wantchitoyo atachira. |
Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.
Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anachiritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.
Ndipo kunali, katapita kamphindi, Iye anapita kumzinda, dzina lake Naini; ndipo ophunzira ake ndi mpingo waukulu wa anthu anapita naye.
Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeze, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere.