Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe mu Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso.
Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga padzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii.
Ndipo Yesu anayendayenda mu Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.
Ndipo kunali tsiku la Sabata, Iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m'manja mwao, nadya.
Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.