Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata;
Luka 6:5 - Buku Lopatulika Ndipo Iye ananena kwa iwo, kuti, Mwana wa Munthu ali Mbuye wa tsiku la Sabata. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye ananena kwa iwo, kuti, Mwana wa Munthu ali Mbuye wa tsiku la Sabata. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu popitiriza adaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu ndi Ambuye wa Sabata.” |
Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata;
Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munatuluka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.
kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha?
Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, Iye analowa m'sunagoge, naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lake lamanja linali lopuwala.
Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,