Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.
Luka 6:44 - Buku Lopatulika Pakuti mtengo uliwonse uzindikirika ndi chipatso chake. Pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti mtengo uliwonse uzindikirika ndi chipatso chake. Pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtengo uliwonse umadziŵika ndi zipatso zake. Sathyola nkhuyu pa minga, kapenanso mphesa pa mtula. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake. Anthu sathyola nkhuyu pa mtengo waminga, kapena mphesa pa nthungwi. |
Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake chomwe chiipa; pakuti ndi chipatso chake mtengo udziwika.
Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.
Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;