Luka 6:34 - Buku Lopatulika Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti inde anthu ochimwa amakongoletsa kwa ochimwa anzao, kuti alandirenso momwemo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti inde anthu ochimwa amakongoletsa kwa ochimwa anzao, kuti alandirenso momwemo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo ngati mukongoza okhawo amene mukudziŵa kuti adzakubwezerani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakongoza anzao ochimwa, kuti akalandirenso momwemo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse. |
Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti anthu ochimwa omwe amachita chomwecho.
Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.