Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu;
Luka 6:2 - Buku Lopatulika Koma Afarisi ena anati, Muchitiranji chosaloledwa kuchitika tsiku la Sabata? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Afarisi ena anati, Muchitiranji chosaloledwa kuchitika tsiku la Sabata? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Afarisi ena adafunsa kuti, “Bwanji mukuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ena mwa Afarisi anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mukuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata?” |
Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu;
Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu.
Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe.
Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kuchita kukondwerera kwako tsiku langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osachita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;
Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata.
Ndipo Afarisi ananena ndi Iye, Taona, achitiranji chosaloleka kuchitika tsiku la Sabata?
Ndipo iwo anati kwa Iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.