Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
Luka 6:16 - Buku Lopatulika ndi Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Iskariote, amene anali wompereka Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Iskariote, amene anali wompereka Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yudasi (mwana wa Yakobe) ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.) Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikarioti amene anamupereka. |
Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani,
Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya yense ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao;
Yudasi, si Iskariote, ananena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi?
alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.
Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu: