Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.
Luka 5:5 - Buku Lopatulika Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Simoni adati, “Aphunzitsi, usiku wonsewu takhalira kugwira ntchito, osapha kanthu, koma chifukwa Inuyo mwatero, chabwino ndiponya makoka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Simoni anayankha kuti, “Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka.” |
Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za mu Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.
Ndipo anadza kwa Iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa bata.
Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana.
Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena.
Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe.
Simoni Petro ananena nao, Ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anatuluka, nalowa m'ngalawa; ndipo mu usiku muja sanagwire kanthu.