Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.
Luka 5:39 - Buku Lopatulika Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Ndipo munthu akangolaŵa vinyo wakale, watsopano sangamufune. Pajatu amati, ‘Wakale ndiye vinyo chaiye.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo palibe amene atamwa vinyo wakale amafuna watsopano, pakuti amati, ‘Wakale ndi okoma.’ ” |
Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.
Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako.
Ndipo kunali tsiku la Sabata, Iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m'manja mwao, nadya.