Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani? Kuti ndadwala ndi chikondi.
Luka 5:34 - Buku Lopatulika Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu anawayankha kuti, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya pamene mkwati ali pakati pawo? |
Ndikulumbirirani, ana aakazi inu a ku Yerusalemu, mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani? Kuti ndadwala ndi chikondi.
Bwenzi lako wapita kuti, mkaziwe woposa kukongola? Bwenzi lako wapatukira kuti, tikamfunefune pamodzi nawe?
Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.
Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.
Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.
Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wake phwando la ukwati,
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.
Ndipo iwo anati kwa Iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.
Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo.
Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.
Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.