Luka 5:25 - Buku Lopatulika Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kunka kunyumba kwake, wakulemekeza Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kunka kunyumba kwake, wakulemekeza Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pomwepo wodwalayo adadzukadi onse akupenya, ndipo adatenga machira aja amene adaagonapo, namapita kwao akutamanda Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu. |
Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.
Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere.
Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinazione ndi kale lonse.
Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko.
Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye.
Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa.