Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.
Luka 5:23 - Buku Lopatulika Chapafupi nchiti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chapafupi nchiti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chapafupi koposa nchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, yamba kuyenda?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi chapafupi ndi chiti: kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo yenda?’ ” |
Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.
Pakuti chapafupi nchiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka. Nuyende?
Chapafupi nchiti, kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende?
Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m'mitima yanu?
Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali nayo mphamvu padziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.