Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 5:19 - Buku Lopatulika

Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa tsindwi, namtsitsira iye poboola pa tsindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa chindwi, namtsitsira iye poboola pa chindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma chifukwa anthu adaachuluka, sadapeze poloŵera naye. Motero adakwera pa denga, nachotsapo mapale ena, nkumutsitsa ndi machira ake omwe kumufikitsa pansi pakati pa anthu, pamaso pa Yesu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Atalephera kupeza njira yochitira zimenezi chifukwa cha gulu la anthu, anakwera naye pa denga ali pa mphasa pomwepo ndi kumutsitsira mʼkati pakati pa gulu la anthu, patsogolo penipeni pa Yesu.

Onani mutuwo



Luka 5:19
7 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana.


ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.


Chimene ndikuuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m'khutu, muchilalikire pa matsindwi a nyumba.


iye ali pamwamba pa tsindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwake;


Ndipo pamene sanakhoze kufika kuli Iye, chifukwa cha khamu la anthu, anasasula tsindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo.


Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu.


Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumzinda, iye anakamba ndi Saulo pamwamba pa nyumba yake.