Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Luka 5:18 - Buku Lopatulika Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono kudafika anthu ena ndi munthu wofa ziwalo, atamnyamulira pa machira. Adayesa kuloŵa naye m'nyumba kuti amkhazike pamaso pa Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amuna ena anabwera atanyamula munthu wofa ziwalo pa mphasa ndipo anayesa kumulowetsa mʼnyumba kuti amugoneke pamaso pa Yesu. |
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali nayo mphamvu padziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.
Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje.