Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha.
Luka 5:16 - Buku Lopatulika Koma Iye anazemba, nanka m'mapululu, nakapemphera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Iye anazemba, nanka m'mapululu, nakapemphera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Iye adapita kumalo kosapitapita anthu, namakapemphera kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Yesu nthawi zambiri ankachoka kupita ku malo a yekha kukapemphera. |
Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha.
Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka,
Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.
Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera.
Ndipo m'kupemphera kwake, maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira.
Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha.