Luka 5:15 - Buku Lopatulika Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe mbiri ya Yesu inkawandirawandira, ndipo makamu ambiri a anthu ankasonkhana kuti amve mau ake, ndiponso kuti aŵachize nthenda zao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mbiri yake inafalikirabe kwambiri kotero kuti magulu a anthu anabwera kudzamvetsera ndi kuti achiritsidwe ku matenda awo. |
Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.
Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya,
Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.
Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala.
Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizingathe kubisika.