Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.
Luka 5:11 - Buku Lopatulika Ndipo m'mene iwo anakocheza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mene iwo anakocheza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero, atakokera zombozo ku mtunda, adasiya zonse namatsata Yesu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye. |
Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine.
Pomwepo Petro anayankha, nati kwa Iye, onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani?
Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.
Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.