Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.
Luka 4:32 - Buku Lopatulika chifukwa mau ake anali ndi ulamuliro. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chifukwa mau ake anali ndi ulamuliro. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankalankhula moonetsa ulamuliro ngati mwiniwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anadabwa ndi chiphunzitso chake chifukwa uthenga wake unali ndi ulamuliro. |
Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.
Ndipo m'sunagoge munali munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuula ndi mau olimba, kuti,
Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.
Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.
koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.
kuti Uthenga Wabwino wathu sunadze kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.