Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.
Luka 4:31 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mzinda wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu adapita ku Kapernao, mudzi wina wa ku Galileya, nkumaphunzitsa pa tsiku la Sabata. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Iye anapita ku Kaperenawo, mudzi wa ku Galileya, ndipo pa Sabata anayamba kuphunzitsa anthu. |
Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.
ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye mu Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali:
Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.
Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mzindawo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao.