Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu, chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.
Luka 4:22 - Buku Lopatulika Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu onse adamtamanda, nkumadabwa ndi mau ogwira mtima amene Iye ankalankhula. Anthuwo ankati, “Kodi uyu si mwana uja wa Yosefeyu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onse anayankhula zabwino za Iye ndipo anadabwa ndi mawu ogwira moyo amene anatuluka mʼkamwa mwake. Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu si mwana wa Yosefe?” |
Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu, chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.
Ndipo pindulani, mu ukulu wanu yendani, kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo; ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.
M'kamwa mwake muli mokoma; inde, ndiye wokondweretsa ndithu. Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa, ana aakazi inu a ku Yerusalemu.
Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.
Ndipo m'mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa.
Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.
Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.
Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba?
mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.