Ndipo adzachitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati, Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse.
Luka 4:21 - Buku Lopatulika Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adaŵauza kuti, “Lero zachitikadi zimene adaaneneratu Malembo amene mwamvaŵa.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anawawuza kuti, “Lero malemba awa akwaniritsidwa mmene mwamveramu.” |
Ndipo adzachitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati, Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse.
Ndipo m'mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa Iye.
Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?
Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo;
Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Khristu, Iye anakwaniritsa chotero.