Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.
Luka 3:20 - Buku Lopatulika anaonjeza pa zonsezi ichinso, kuti anatsekera Yohane m'nyumba yandende. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 anaonjeza pa zonsezi ichinso, kuti anatsekera Yohane m'nyumba yandende. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake, kuwonjezera pa zonsezi, Herode adatsekera Yohaneyo m'ndende. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Herode anawonjezanso choyipa ichi pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende. |
Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza mu Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova.
ndiponso chifukwa cha mwazi wosachimwa adaukhetsa; popeza anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa; ndipo Yehova sanafune kukhululukira.
koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.
Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.
Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.
popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.