Luka 3:19 - Buku Lopatulika Koma Herode mfumu ija, m'mene Yohane anamdzudzula chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndi cha zinthu zonse zoipa Herode anazichita, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Herode mfumu ija, m'mene Yohane anamdzudzula chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndi cha zinthu zonse zoipa Herode anazichita, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komanso adadzudzula mfumu Herode chifukwa chokwatira Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndiponso chifukwa cha zoipa zina zambiri zimene ankachita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma pamene Yohane anadzudzula Herode wolamulirayo chifukwa chokwatira Herodia, mkazi wa mʼbale wake, ndi zoyipa zina zonse anazichita, |
Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau,
Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode.
Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;