Luka 3:14 - Buku Lopatulika Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Asilikali omwe adamufunsa kuti, “Nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.” |
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.
Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.
Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka;
kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,
Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo.
Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;
Ndipo ndinamva mau aakulu mu Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku.