Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.
Luka 24:7 - Buku Lopatulika ndi kunena, kuti, Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ochimwa, ndi kupachikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lachitatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi kunena, kuti, Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ochimwa, ndi kupachikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lachitatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja adaakuuzani kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja mwa anthu ochimwa, kupachikidwa pa mtanda, ndi kuuka kwa akufa patapita masiku atatu.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ ” |
Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa.
ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu;