Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,
Luka 24:52 - Buku Lopatulika Ndipo anamlambira Iye, nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamlambira Iye, nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo anamulambira Iye ndipo anabwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. |
Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,
Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, namgwadira.
Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine.
Ndipo inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu.
Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu.
Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kuchokera kuphiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata.
amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero: