Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye, koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.
Luka 24:41 - Buku Lopatulika Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe, ndipo adaathedwa nzeru. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi pano muli nako kanthu kakudya?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” |
Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye, koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga.
Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereze iwo amene adamuona, atauka Iye.
Ndipo inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu.
Ndipo pozindikira mau ake a Petro, chifukwa cha kukondwera sanatsegule pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo.