Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.
Luka 24:34 - Buku Lopatulika nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa akunena kuti, “Ambuye adaukadi, ndipo Simoni waŵaona.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anati, “Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni.” |
Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu.
Palibe kuno Iye, komatu anauka; kumbukirani muja adalankhula nanu, pamene analinso mu Galileya,
Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.
Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?
kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;