Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.
Luka 24:23 - Buku Lopatulika ndipo m'mene sanapeze mtembo wake, anadza, nanena kuti adaona m'masomphenya angelo, amene ananena kuti ali ndi moyo Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo m'mene sanapeze mtembo wake, anadza, nanena kuti adaona m'masomphenya angelo, amene ananena kuti ali ndi moyo Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndiye amati sadaupeze mtembo wake. Tsono atabwerako amadzasimba kuti anaona angelo amene anaŵauza kuti Yesu ali moyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo. |
Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye.
Ndipo ena a iwo anali nafe anachoka kunka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sanamuone.
Maria wa Magadala anapita, nalalikira kwa ophunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye.