Luka 24:13 - Buku Lopatulika Ndipo taonani, awiri a mwa iwo analikupita tsiku lomwelo kumudzi dzina lake Emausi, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo taonani, awiri a mwa iwo analikupita tsiku lomwelo kumudzi dzina lake Emausi, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku lomwelo ophunzira aŵiri ankapita ku mudzi wotchedwa Emausi. Kuchokera ku Emausi kufika ku Yerusalemu ndi mtunda wokwanira ngati makilomita khumi ndi limodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu. |
Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lake Kleopa, anayankha nati kwa Iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo mu Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano?