Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.
Luka 24:12 - Buku Lopatulika Koma Petro ananyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama anaona nsalu zabafuta pazokha; ndipo anachoka nanka kwao, nazizwa ndi chija chidachitikacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Petro ananyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama anaona nsalu zoyera pa zokha; ndipo anachoka nanka kwao, nazizwa ndi chija chidachitikacho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe Petro adanyamuka nathamangira ku manda. Adaŵeramiramo naona nsalu zamaliro zokha, kenaka nkubwerera kunyumba akudabwa ndi zimene zidaachitikazo.] Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo. |
Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda.